2 Mngelo uja anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?”
3 Ndipo mngeloyo anandiwuza kuti, “Awa ndi matemberero amene akupita pa dziko lonse lapansi; potsata zimene zalembedwa mʼkati mwa chikalatamo, aliyense wakuba adzachotsedwa, ndipo potsata zomwe zalembedwa kunja kwake, aliyense wolumbira zabodza adzachotsedwanso. 4 Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza, ndipo lidzalowa mʼnyumba ya munthu wakuba ndi munthu wolumbira zabodza mʼdzina langa. Lidzakhala mʼnyumbamo mpaka kuyiwonongeratu, matabwa ake ndi miyala yake yomwe.’ ”
6 Ndinafunsa kuti, “Kodi chimenechi nʼchiyani?”
7 Pamenepo chovundikira chake chamtovu chinatukulidwa, ndipo mʼdengumo munali mutakhala mkazi. 8 Mngeloyo anati, “Chimenechi ndi choyipa,” ndipo anamukankhira mkaziyo mʼdengu muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake.
9 Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi.
10 Ine ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Dengulo akupita nalo kuti?”
11 Iye anayankha kuti, “Ku dziko la Babuloni kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzayikamo dengulo.”
<- ZEKARIYA 4ZEKARIYA 6 ->