1 Chizindikiro chachikulu chinaoneka kuthambo; mayi atavala dzuwa, mapazi ake ataponda mwezi, pamutu pake pali chipewa chaufumu chokhala ndi nyenyezi khumi ndi ziwiri. 2 Mayiyo anali woyembekezera ndipo pa nthawi yake yochira analira mokuwa chifukwa cha ululu wakubala. 3 Kenaka ku thambo kunaonekanso chizindikiro china; chinjoka chachikulu kwambiri, chofiira chomwe chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi; pamutu uliwonse chitavala chipewa chaufumu. 4 Mchira wake unakokolola gawo limodzi la magawo atatu a nyenyezi kuzichotsa ku thambo ndi kuziponya pa dziko lapansi. Chinjoka chija chinadzayima patsogolo pa mayi uja amene anali pafupi kuberekayu kuti mwanayo akangobadwa chimudye. 5 Mayiyo anabereka mwana wamwamuna amene adzalamulira anthu a mitundu ina yonse ndi ndodo yachitsulo. Ndipo mwanayo analandidwa ku dzanja la mayiyo ndi kupita naye kwa Mulungu ku mpando wake waufumu. 6 Mayiyo anathawira ku chipululu ku malo kumene Mulungu anamukonzera, kumene akasamalidweko masiku 1,260.
7 Zitatero, kumwamba kunayambika nkhondo. Mikayeli ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho ndi angelo ake anabwezeranso. 8 Koma analibe mphamvu ndipo anagonjetsedwa nathamangitsidwa kumwambako. 9 Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.