Salimo 39
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide.
1 Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga
ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;
ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero
nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”
2 Koma pamene ndinali chete
osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino
mavuto anga anachulukirabe.
3 Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,
ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;
kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:
4 “Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga
ndi chiwerengero cha masiku anga;
mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.
5 Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,
kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;
moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.
Sela
6 Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:
Iye amangovutika koma popanda phindu;
amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.
7 “Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?
Chiyembekezo changa chili mwa Inu.
8 Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;
musandisandutse chonyozeka kwa opusa.
9 Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga
pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.
10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine;
ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.
11 Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;
mumawononga chuma chawo monga njenjete;
munthu aliyense ali ngati mpweya.
Sela
12 “Imvani pemphero langa Inu Yehova,
mverani kulira kwanga kopempha thandizo;
musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,
popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;
monga anachitira makolo anga onse.
13 Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala