Salimo 27
Salimo la Davide.
1 Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
ndidzachita mantha ndi yani?
2 Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane
kudzadya mnofu wanga,
pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo,
iwo adzapunthwa ndi kugwa.
3 Ngakhale gulu lankhondo lindizinge,
mtima wanga sudzaopa.
Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane,
ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.
4 Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,
ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:
kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova
masiku onse a moyo wanga,
ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,
ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
5 Pakuti pa tsiku la msautso
Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo;
adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake
ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
6 Kotero mutu wanga udzakwezedwa
kuposa adani anga amene andizungulira;
pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe;
ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.
7 Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova
mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.
8 Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!”
Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.
9 Musandibisire nkhope yanu,
musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo;
mwakhala muli thandizo langa.
Musandikane kapena kunditaya,
Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
10 Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya
Yehova adzandisamala.
11 Phunzitseni njira yanu Inu Yehova,
munditsogolere mʼnjira yowongoka
chifukwa cha ondizunza.
12 Musandipereke ku zokhumba za adani anga,
pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane
ndipo zikundiopseza.
13 Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;
ndidzaona ubwino wa Yehova
mʼdziko la anthu amoyo.
14 Dikirani pa Yehova;
khalani anyonga ndipo limbani mtima