Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
Salimo 141
Salimo la Davide.
1 Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine.
Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.
2 Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani;
kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
 
3 Yehova ikani mlonda pakamwa panga;
londerani khomo la pa milomo yanga.
4 Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa;
kuchita ntchito zonyansa
pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa;
musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.
 
5 Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo;
andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga.
Mutu wanga sudzakana zimenezi.
 
Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.
6 Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri,
ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino.
7 Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza,
ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.”
 
8 Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse;
ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa.
9 Mundipulumutse ku misampha imene anditchera,
ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera.
10 Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo,
mpaka ine nditadutsa mwamtendere.

<- MASALIMO 140MASALIMO 142 ->