Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
Salimo 134
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
1 Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova,
amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova.
2 Kwezani manja anu mʼmalo opatulika
ndipo mutamande Yehova.
 
3 Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
akudalitseni kuchokera mʼZiyoni.

<- MASALIMO 133MASALIMO 135 ->