Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
Salimo 130
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
1 Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
2 Ambuye imvani mawu anga.
Makutu anu akhale tcheru kumva
kupempha chifundo kwanga.
 
3 Inu Yehova, mukanamawerengera machimo,
Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?
4 Koma kwa Inu kuli chikhululukiro;
nʼchifukwa chake mumaopedwa.
 
5 Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,
ndipo ndimakhulupirira mawu ake.
6 Moyo wanga umayembekezera Ambuye,
kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
 
7 Yembekeza Yehova, iwe Israeli,
pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika
ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
8 Iye mwini adzawombola Israeli
ku machimo ake onse.

<- MASALIMO 129MASALIMO 131 ->