Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
Salimo 13
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
1 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?
Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
2 Ndidzalimbana ndi maganizo anga
ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?
Mpaka liti adani anga adzandipambana?
 
3 Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.
Walitsani maso anga kuti ndingafe;
4 mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”
ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.
 
5 Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;
mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
6 Ine ndidzayimbira Yehova
pakuti wandichitira zokoma.

<- MASALIMO 12MASALIMO 14 ->