Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
BUKU LACHISANU
107
Masalimo 107–150
1 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
2 Owomboledwa a Yehova anene zimenezi
amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
3 iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,
kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.
 
4 Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu,
osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.
5 Iwo anamva njala ndi ludzu,
ndipo miyoyo yawo inafowokeratu.
6 Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awo
ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
7 Iye anawatsogolera mʼnjira yowongoka
kupita ku mzinda umene anakakhazikikako.
8 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
9 pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzu
ndipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino.
 
10 Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu,
amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo,
11 pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu
ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba.
12 Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga;
anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize.
13 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
14 Yehova anawatulutsa mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu
ndipo anadula maunyolo awo.
15 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
16 pakuti Iye amathyola zipata zamkuwa
ndi kudula pakati mipiringidzo yachitsulo.
 
17 Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira,
ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.
18 Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse
ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.
19 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.
20 Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;
anawalanditsa ku manda.
21 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
22 Apereke nsembe yachiyamiko
ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.
 
23 Ena anayenda pa nyanja mʼsitima zapamadzi;
Iwo anali anthu amalonda pa nyanja yayikulu.
24 Anaona ntchito za Yehova,
machitidwe ake odabwitsa mʼnyanja yakuya.
25 Pakuti Iye anayankhula ndi kuwutsa mphepo yamkuntho
imene inabweretsa mafunde ataliatali.
26 Sitima za pamadzizo zinatukulidwa mmwamba ndi kutsikira pansi pakuya;
pamene amawonongeka, kulimba mtima kwawo kunasungunuka.
27 Anachita chizungulire ndi kudzandira ngati anthu oledzera;
anali pa mapeto a moyo wawo.
28 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
ndipo Iyeyo anawapulumutsa ku masautso awo.
29 Yehova analetsa namondwe,
mafunde a mʼnyanja anatontholetsedwa.
30 Anali osangalala pamene kunakhala bata,
ndipo Iye anawatsogolera ku dooko limene amalifuna.
31 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
32 Akuze Iye mu msonkhano wa anthu
ndi kumutamanda pabwalo la akuluakulu.
 
33 Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu,
akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma,
34 ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere,
chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.
35 Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzi
ndi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda;
36 kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako,
ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko.
37 Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesa
ndipo anakolola zipatso zochuluka;
38 Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri,
ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe.
 
39 Kenaka chiwerengero chawo chinachepa ndipo iwo anatsitsidwa
chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni;
40 Iye amene amakhuthulira mʼnyozo pa olemekezeka
anawachititsa kuyendayenda mʼmalo owumawo wopanda njira.
41 Koma Iyeyo anakweza anthu osowa kuchoka ku masautso awo
ngati magulu a nkhosa.
42 Anthu olungama mtima amaona ndi kusangalala,
koma anthu onse oyipa amatseka pakamwa pawo.
 
43 Aliyense wanzeru asamalitse zinthu zimenezi
ndi kuganizira za chikondi chachikulu cha Yehova.

<- MASALIMO 106MASALIMO 108 ->