Salimo 10
1 Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali?
Chifukwa chiyani mukudzibisa nokha pa nthawi ya mavuto?
2 Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka,
amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza.
3 Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake;
amadalitsa aumbombo ndi kuchitira chipongwe Yehova.
4 Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu;
mʼmaganizo ake wonse mulibe malo a Mulungu.
5 Zinthu zake zimamuyendera bwino;
iye ndi wamwano ndipo malamulo anu ali nawo kutali;
amanyogodola adani ake onse.
6 Iye amadziyankhulira kuti, “Palibe chimene chidzandigwedeze.
Ndidzakhala wokondwa nthawi zonse ndipo sindidzakhala pa mavuto.”
7 Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza;
zovutitsa ndi zoyipa zili pansi pa lilime lake.
8 Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi,
kuchokera pobisalapo amapha anthu osalakwa,
amayangʼanayangʼana mwachinsinsi anthu oti awawononge.
9 Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba.
Amabisalira kuti agwire anthu opanda mphamvu;
amagwira anthu opanda mphamvu ndi kuwakokera mu ukonde wake.
10 Anthuwo amawapondaponda ndipo amakomoka;
amakhala pansi pa mphamvu zake.
11 Iye amati mu mtima mwake, “Mulungu wayiwala,
wabisa nkhope yake ndipo sakuonanso.”
12 Dzukani Yehova! Onetsani dzanja lanu Inu Mulungu.
Musayiwale anthu opanda mphamvu.
13 Nʼchifukwa chiyani munthu woyipa amachitira chipongwe Mulungu?
Chifukwa chiyani amati mu mtima mwake,
“Iye sandiyimba mlandu?”
14 Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa,
mumaganizira zochitapo kanthu.
Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti
Inu ndi mthandizi wa ana amasiye.
15 Thyolani dzanja la woyipitsitsa ndi la munthu woyipa;
muzengeni mlandu chifukwa cha zoyipa zake
zimene sizikanadziwika.
16 Yehova ndi Mfumu kwamuyaya;
mitundu ya anthu idzawonongeka kuchoka mʼdziko lake.
17 Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa;
mumawalimbikitsa ndipo mumamva kulira kwawo.
18 Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa,