1 Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti, 2 “Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi. 3 Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali. 4 Munthu mmodzi wochokera ku fuko lililonse yemwe ndi mtsogoleri wa banja lake, ndiye akuthandizeni pa ntchitoyi. 5 Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa:
Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni,
6 Selumieli mwana wa Zurisadai, kuchokera ku fuko la Simeoni,
7 Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda,
8 Netanieli mwana wa Zuwara, kuchokera ku fuko la Isakara,
9 Eliabu mwana wa Heloni, kuchokera ku fuko la Zebuloni,
10 Mwa ana a Yosefe:
kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi;
kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri;
11 Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini,
12 Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani,
13 Pagieli mwana wa Okirani, kuchokera ku fuko la Aseri,
14 Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi,
15 Ahira mwana wa Enani, kuchokera ku fuko la Nafutali.”
16 Amenewa ndi anthu amene anasankhidwa kuchokera mʼmagulu mwawo, eni mbumba a mafuko a makolo awo. Iwowa anali atsogoleri a mafuko a Israeli.
17 Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa, 18 ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi 19 monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:
20 Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 21 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500.
22 Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 23 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300.
24 Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 25 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650.
26 Kuchokera mwa zidzukulu za Yuda:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 27 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.
28 Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 29 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.
30 Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 31 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.
32 Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe:
Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 33 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.
34 Kuchokera mwa zidzukulu za Manase:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 35 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200.
36 Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 37 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400.
38 Kuchokera mwa zidzukulu za Dani:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 39 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700.
40 Kuchokera mwa zidzukulu za Aseri:
Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 41 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500.
42 Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali:
Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo. 43 Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400.
44 Amenewa ndiwo anthu amene Mose ndi Aaroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri khumi ndi awiri a Israeli, aliyense kuyimira fuko lake. 45 Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo. 46 Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550.
47 Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena. 48 Pakuti Yehova anawuza Mose kuti, 49 “Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli. 50 Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo. 51 Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa. 52 Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake. 53 Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.”