1 Iye atatsika ku phiri kuja, anthu ambirimbiri anamutsata. 2 Ndipo munthu wakhate anadza kwa Yesu namugwadira nati, “Ambuye, ngati mufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
3 Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati,
5 Yesu atalowa mʼKaperenamu, Kenturiyo anabwera kwa Iye napempha chithandizo, 6 nati, “Ambuye, wantchito wanga ali chigonere ku nyumba, sakuthanso kuyenda, akumva kuwawa kwambiri.”
7 Ndipo Yesu anati kwa iye,
8 Kenturiyo uja anayankha kuti, “Ambuye, ndine wosayenera kuti Inu mukalowe mʼnyumba mwanga. Koma mungonena mawu ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa. 9 Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita.”
10 Yesu atamva zimenezi, anadabwa ndipo anati kwa omutsatira,
13 Pamenepo Yesu anati kwa Kenturiyo,
14 Ndipo Yesu atalowa mʼnyumba ya Petro, anaona mpongozi wake wa Petro ali gone akudwala malungo. 15 Ndipo Yesu anakhudza dzanja lake ndipo pomwepo anachira nayamba kumutumikira.
16 Itafika nthawi yamadzulo, anthu anabweretsa kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda ndipo anatulutsa ziwandazo ndi mawu okha, nachiritsa odwala onse. 17 Uku kunali kukwaniritsa zimene ananena mneneri Yesaya kuti,
18 Yesu ataona gulu la anthu litamuzungulira, analamula kuti awolokere kutsidya lina la nyanja. 19 Ndipo mphunzitsi wa malamulo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ine ndidzakutsatani kulikonse kumene muzipita.”
20 Yesu anayankha kuti,
21 Wophunzira wina anati kwa Iye, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakayika maliro a abambo anga.”
22 Koma Yesu anamuwuza kuti,
23 Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira. 24 Ndipo taonani mwadzidzidzi mphepo yayikulu yamkuntho inawomba pa nyanjapo, kotero kuti bwatolo linayamba kumizidwa ndi mafunde. Koma Yesu anali mtulo. 25 Ophunzira ake anapita namudzutsa nati, “Ambuye! Tipulumutseni! Tikumira!”
26 Iye anawayankha kuti,
27 Ndipo ophunzirawo anadabwa nafunsa kuti, “Ndi munthu wotani uyu? Kuti ngakhale mphepo ndi mafunde zimvera Iye!”
28 Ndipo atafika ku mbali ina ya dera la Gadara, anakumana ndi anthu awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera ku manda. Iwowa anali woopsa kwambiri kotero kuti panalibe munthu akanatha kudzera njira imeneyo. 29 Ndipo iwo anafuwulira kwa Yesu nati, “Mukufuna chiyani kwa ife, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthawi yake isanafike?”
30 Ndipo patali pake panali gulu la nkhumba zimene zimadya. 31 Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, “Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo.”
32 Iye anati kwa ziwandazo,