Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
26
Chiwembu cha Ayuda pa Yesu
1 Yesu atamaliza kuyankhula zonsezi, anati kwa ophunzira ake, 2 “Monga mukudziwa, kwatsala masiku awiri kuti Paska ifike ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti apachikidwe.”

3 Pamenepo akulu a ansembe ndi akuluakulu anasonkhana ku nyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa, 4 ndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha. 5 Ndipo anati, “Osati nthawi yaphwando chifukwa pangabuke chipolowe pakati pa anthu.”

Yesu Adzozedwa ku Betaniya
6 Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate, 7 mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.

8 Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? 9 Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.”

10 Yesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 11 Osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 12 Pamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 13 Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.”

Yudasi Avomereza Kupereka Yesu
14 Pamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe 15 nafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu. 16 Kuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu.
Paska Womaliza ndi Mgonero wa Ambuye
17 Pa tsiku loyamba laphwando la buledi wopanda yisiti, ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonze kuti malo odyera Paska?”

18 Iye anayankha kuti, “Pitani mu mzinda kwa munthu wakutiwakuti ndipo kamuwuzeni kuti, ‘Aphunzitsi akuti, nthawi yanga yoyikidwa yayandikira. Ine ndidzadya phwando la Paska ndi ophunzira anga ku nyumba kwako.’ ” 19 Pamenepo ophunzira ake anachita monga momwe Yesu anawawuzira ndipo anakonza Paska.

20 Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi awiriwo anakhala pa tebulo nʼkumadya. 21 Akudya, Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka.”

22 Iwo anamva chisoni kwambiri ndipo anayamba kuyankhulana naye mmodzimmodzi nati, “Kodi nʼkukhala ine Ambuye?”

23 Yesu anayankha nati, “Iye amene akusunsa mʼmbale pamodzi ndi Ine, yemweyo adzandipereka. 24 Mwana wa Munthu adzaphedwa monga mmene kunalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene apereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”

25 Ndipo Yudasi amene anamupereka Iye anati, “Monga nʼkukhala ine Aphunzitsi?”

Yesu anayankha nati, “Iwe watero.”

26 Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, idyani; ili ndi thupi langa.”

27 Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati, “Imwani nonsenu. 28 Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri kuti akhululukidwe machimo. 29 Ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mtengo wa mpesa kuyambira lero mpaka tsiku ilo pamene ndidzamwenso mwatsopano ndi inu mu ufumu wa Atate anga.”

30 Atayimba nyimbo, anatuluka kupita ku phiri la Olivi.

Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana
31 Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Usiku omwe uno inu nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa:
“ ‘Kantha mʼbusa,
ndipo nkhosa zidzabalalika.’
32 Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”

33 Petro anayankha nati, “Ngakhale onsewa atakuthawani, ine ndekha ayi.”

34 Yesu anayankha nati, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti usiku omwe uno, asanalire tambala, udzandikana Ine katatu.”

35 Koma Petro ananenetsa nati, “Ngakhale kutakhala kufa nanu pamodzi, sindidzakukanani.” Ndipo ophunzira onse ananena chimodzimodzi.

Yesu mu Getsemani
36 Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti, “Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera apo.” 37 Anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo, ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika mu mtima. 38 Pamenepo anawawuza kuti, “Moyo wanga uli ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo dikirani pamodzi ndi Ine.”

39 Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti, “Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu.”

40 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti, “Kodi anthu inu, simukanakhala maso pamodzi ndi Ine kwa ora limodzi lokha? 41 Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.”

42 Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti, “Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike.”

43 Atabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo. 44 Choncho anawasiya napitanso kukapemphera kachitatu nanenanso chimodzimodzi.

45 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo, “Kodi mukanagonabe ndi kupumula? Taonani, ora layandikira ndipo Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa ochimwa. 46 Imirirani, tiyeni tizipita! Wondipereka Ine wafika!”

Amugwira Yesu
47 Akuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu. 48 Womuperekayo anawawuziratu chizindikiro anthuwo kuti, “Amene ndidzapsompsona ndi iyeyo; mugwireni.” 49 Pamenepo Yudasi anapita kwa Yesu nati, “Moni, Aphunzitsi!” Ndipo anapsompsona Iye.

50 Yesu anayankha kuti, “Bwenzi langa, chita chimene wabwerera.”

Pamenepo anthuwo anabwera patsogolo namugwira Yesu ndi kumumanga. 51 Pa chifukwa ichi, mmodzi wa anzake a Yesu anagwira lupanga lake, nalisolola ndi kutema wantchito wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake.

52 Yesu anati kwa iye, “Bwezera lupanga lako mʼchimake, chifukwa onse amene amapha ndi lupanga adzafa ndi lupanga. 53 Kodi mukuganiza kuti sindingathe kupempha Atate anga ndipo nthawi yomweyo nʼkundipatsa magulu a angelo oposa khumi ndi awiri? 54 Koma nanga malemba akwaniritsidwa bwanji amene akuti ziyenera kuchitika motere?”

55 Pa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo, “Kodi ndine mtsogoleri wa anthu owukira kuti mwabwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mʼNyumba ya Mulungu kuphunzitsa, koma simunandigwire. 56 Koma zonsezi zachitika kuti zolembedwa ndi aneneri zikwaniritsidwe.” Pamenepo ophunzira anamusiya nathawa.

Yesu ku Bwalo la Akulu Ayuda
57 Iwo amene anamugwira Yesu anamutengera kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anasonkhana. 58 Koma Petro anamutsatira Iye patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Analowa nakhala pansi pamodzi ndi alonda kuti aone zotsatira.

59 Akulu a ansembe ndi akulu olamulira Ayuda amafunafuna umboni wonama wofuna kuphera Yesu. 60 Koma sanathe kupeza uliwonse, angakhale kuti mboni zambiri zabodza zinapezeka.

Pomalizira mboni ziwiri zinabwera patsogolo. 61 Ndipo zinati, “Munthu uyu anati, ‘Ndikhoza kupasula Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso mʼmasiku atatu.’ ”

62 Pamenepo mkulu wa ansembe anayimirira nati kwa Yesu, “Kodi suyankha? Kodi umboni umenewu ndi otani umene anthu awa akupereka kukutsutsa Iwe?” 63 Koma Yesu anakhalabe chete.

Mkulu wa ansembe anati kwa Iye, “Ndikulamulira Iwe ndi lumbiro pamaso pa Mulungu wa Moyo: utiwuze ife ngati ndiwe Khristu Mwana wa Mulungu.”

64 Yesu anayankha nati, “Mwanena ndinu. Koma ndikunena kwa inu nonse: mʼtsogolomo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera ndi mitambo ya kumwamba.”

65 Pamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake. 66 Mukuganiza bwanji?”

Iwo anayankha kuti, “Ayenera kuphedwa!”

67 Kenaka anamulavulira kumaso namumenya ndi zibakera. Ena anamumenya makofi. 68 Ndipo anati, “Tanenera kwa ife, Khristu. Wakumenya ndani?”

Petro Amukana Yesu
69 Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”

70 Koma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.”

71 Kenaka anachoka kupita ku khomo la mpanda, kumene mtsikana wina anamuonanso nawuza anthu nati, “Munthu uyu anali ndi Yesu wa ku Nazareti.”

72 Iye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!”

73 Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.”

74 Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!”

Nthawi yomweyo tambala analira. 75 Ndipo Petro anakumbukira mawu amene Yesu anayankhula kuti, “Tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.” Ndipo anatuluka panja nakalira kwambiri.

<- MATEYU 25MATEYU 27 ->