1 Yesu anayankhula nawonso mʼmafanizo, nati, 2“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna.3Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.
4“Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’
5“Koma iwo sanalabadire ndipo anachoka; wina anapita ku munda wake ndi wina ku malonda ake.6Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha.7Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.
8“Pamenepo anati kwa antchito ake, ‘Phwando laukwati lakonzedwa, koma amene ndinawayitana sanali oyenera.9Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’10Pamenepo antchitowo anapita ku misewu nakasonkhanitsa anthu onse amene anakawapeza, abwino ndi oyipa omwe, ndipo nyumba ya madyerero inadzaza ndi oyitanidwa.
13“Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’
14“Popeza oyitanidwa ndi ambiri koma osankhidwa ndi ochepa.”
Za Kupereka Msonkho
15 Kenaka Afarisi anatuluka nakakonza njira zomupezera zifukwa Yesu mʼmawu ake. 16 Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani? 17 Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”
18 Koma Yesu podziwa maganizo awo oyipa anati, “Inu achiphamaso, bwanji mufuna kundipezera chifukwa?19Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari, 20 ndipo anawafunsa kuti, “Kodi chithunzi ichi ndi malemba awa ndi za ndani?”
21 Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.”
Pamenepo anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
23 Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso. 24 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 25 Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo. 26 Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri. 27 Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso. 28 Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?”
29 Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu.30Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba.31Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,32‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”
33 Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.
Lamulo Lalikulu Koposa
34 Pakumva kuti Yesu anawakhalitsa chete Asaduki, Afarisi anasonkhana pamodzi. 35 Mmodzi wa iwo, katswiri wa malamulo anamuyesa Iye ndi funso ndipo anati, 36 “Aphunzitsi, kodi lamulo lalikulu koposa mu malamulo ndi liti?” 37 Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse.38Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse.39Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’40Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”
Kodi Khristu ndi Mwana wa Ndani?
41 Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti, 42“Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?”
Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.”
43 Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,