nditadzabwezeretsanso Yerusalemu ndi Yuda mʼchimake,
2 ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse
ndipo ndidzawabweretsa ku Chigwa cha Yehosafati.
Kumeneko ndidzawaweruza
chifukwa cha cholowa changa, anthu anga Aisraeli,
pakuti anabalalitsa anthu anga pakati pa mitundu ya anthu
ndikugawa dziko langa.
3 Anagawana anthu anga pochita maere
ndipo anyamata anawasinthanitsa ndi akazi achiwerewere;
anagulitsa atsikana chifukwa cha vinyo
kuti iwo amwe.
4 “Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu. 5 Pakuti munatenga siliva ndi golide wanga ndi kupita nacho chuma changa chamtengowapatali ku nyumba zanu zopembedzera mafano. 6 Inu munagulitsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kwa Agriki, kuti apite kutali ndi malire a dziko lawo.
7 “Taonani, Ine ndidzawachotsa kumalo kumene munawagulitsako, ndipo ndidzabwezera zimene mwachita pa mitu yanu. 8 Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzawagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali.” Yehova wayankhula.
9 Lengezani izi pakati pa anthu a mitundu ina:
Konzekerani nkhondo!
Dzutsani ankhondo amphamvu!
Asilikali onse afike pafupi ndipo ayambe nkhondo.
10 Sulani makasu anu kuti akhale malupanga
ndipo zikwanje zanu zikhale mikondo.
Munthu wofowoka anene kuti,
“Ndine wamphamvu!”
11 Bwerani msanga, inu anthu a mitundu yonse kuchokera ku mbali zonse,
ndipo musonkhane kumeneko.
Tumizani ankhondo anu Yehova!
12 “Mitundu ya anthu idzuke;
ipite ku Chigwa cha Yehosafati,
pakuti kumeneko Ine ndidzakhala
ndikuweruza anthu a mitundu yonse yozungulira.
13 Tengani chikwakwa chodulira tirigu,
pakuti mbewu zakhwima.
Bwerani dzapondeni mphesa,
pakuti mopsinyira mphesa mwadzaza
ndipo mitsuko ikusefukira;
kuyipa kwa anthuwa nʼkwakukulu kwambiri!”
14 Chigulu cha anthu, chigulu cha anthu,
mʼchigwa cha chiweruzo!
Pakuti tsiku la Yehova layandikira
mʼchigwa cha chiweruzo.
15 Dzuwa ndi mwezi zidzadetsedwa,
ndipo nyenyezi sizidzawalanso.
16 Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyoni
ndipo mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera mu Yerusalemu;
dziko lapansi ndi thambo zidzagwedezeka.
Koma Yehova adzakhala pothawira pa anthu ake,
linga la anthu a ku Israeli.
Madalitso a Anthu a Mulungu
17 “Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wanu,