Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
40
1 Yehova anati kwa Yobu:
2 “Kodi iwe ufuna kukangana ndi Wamphamvuzonse?
Iwe amene unatsutsana ndi Mulungu umuyankhe Iyeyo!”

3 Pamenepo Yobu anayankha Yehova:

4 “Ine sindili kanthu konse,
kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Ndagwira pakamwa panga.
5 Ndinayankhula kamodzi, koma pano ndilibe yankho,
ndinayankha kawiri, koma sindiwonjezeranso mawu ena.”

6 Ndipo Yehova anayankha Yobu mʼkamvuluvulu kuti,

7 “Tsopano vala dzilimbe ngati mwamuna;
ndikufunsa mafunso
ndipo iwe undiyankhe.
 
8 “Kodi iwe unganyoze chiweruzo changa cholungama?
Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?
9 Kodi uli ndi dzanja monga la Mulungu,
ndipo mawu ako angagunde ngati mphenzi monga a Mulungu?
10 Ngati zili choncho udzikometsere ndi ulemerero ndi kukongola,
ndipo udziveke ulemu ndi ulemerero waufumu.
11 Tsanula ukali wako wosefukirawo,
uyangʼane aliyense wodzikuza ndipo umuchepetse,
12 Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse,
uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo.
13 Onsewo uwakwirire pamodzi mfumbi;
ukulunge nkhope zawo mʼmanda.
14 Ukatero Ine ndidzakuvomereza
kuti dzanja lako lamanja lakupulumutsadi.
 
15 “Taganiza za mvuwu,
imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe,
ndipo imadya udzu ngati ngʼombe.
16 Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri,
thupi lake ndi lanyonga kwambiri!
17 Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza;
mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.
18 Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa,
nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.
19 Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu,
komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake.
20 Imapeza chakudya chake ku mtunda
ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake.
21 Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta,
imabisala mʼbango ndiponso pa thawale.
22 Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta;
imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje.
23 Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha,
iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake.
24 Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza
kapena kuyikola mu msampha?