Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
44
Masautso Chifukwa cha Kupembedza Mafano
1 Uthenga umene Yeremiya analandira wonena za Ayuda onse amene ankakhala ku Igupto, ku mizinda ya Migidoli, Tapanesi ndi Mefisi, ndiponso ku Patirosi ndi uwu: 2 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu mwaona mavuto aakulu amene ndinawabweretsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda munthu wokhalamo. 3 Zimenezi zinachitika chifukwa cha zoyipa zomwe anachita. Iwo anaputa mkwiyo wanga pofukiza lubani ndi potumikira milungu ina imene iwo kapena inu ngakhalenso makolo anu sanayidziwe. 4 Kawirikawiri Ine ndakhala ndikutuma atumiki anga, aneneri, amene anati, ‘Musachite chinthu chonyansachi chimene Ine ndimadana nacho!’ 5 Koma iwo sanamvere kapena kulabadira; sanatembenuke kusiya zoyipa zawo kapena kuleka kufukiza lubani kwa milungu ina. 6 Nʼchifukwa chake mkwiyo wanga unayaka ngati moto kutentha mizinda ya ku Yuda ndi misewu ya mu Yerusalemu ndi kuyisandutsa bwinja mpaka lero.

7 “Ndiye tsopano Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, ‘Chifukwa chiyani mukufuna kudziwononga chotere? Kodi mukufuna kuti amuna, akazi, ana ndi makanda onse aphedwe ndi kuti mu Yuda musatsale ndi munthu mmodzi yemwe? 8 Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga popembedza mafano pofukiza lubani kwa milungu ina mʼdziko lino la Igupto mʼmene mukukhalamo. Kodi mukuchita zimenezi kuti mudziwononge nokha ndi kuti mudzisandutse chinthu choseketsa ndi chonyozeka pakati pa mitundu yonse ya dziko lapansi? 9 Kodi mwayiwala zoyipa zimene anachita makolo anu, mafumu a ku Yuda ndi akazi awo, ndiponso zoyipa zimene munachita inuyo ndi akazi anu mʼdziko la Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? 10 Koma mpaka lero simunalape. Simunandilemekeze kapena kumvera malamulo anga amene ndinayikira inuyo ndi makolo anu.

11 “Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Ine ndatsimikiza zobweretsa mavuto pa inu ndi kuwatheratu anthu a ku Yuda. 12 Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene atsimikiza zopita ku Igupto ndi kukakhala kumeneko. Onse adzathera ku Igupto. Adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Adzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, chinthu choseketsa ndi chonyozeka. 13 Ndidzalanga Ayuda okhala ku Igupto ndi lupanga, njala ndi mliri, ngati mmene ndinalangira anthu a ku Yerusalemu. 14 Motero mwa anthu amene anapita ku Igupto palibe ndi mmodzi yemwe adzapulumuke, kapena kukhala ndi moyo, kapena kubwerera ku Yuda. Palibe amene adzabwerere kupatula othawa nkhondo.’ ”

15 Tsono amuna onse amene anadziwa kuti akazi awo ankafukiza lubani kwa milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, gulu lalikulu la anthu, pamodzi ndi anthu onse amene amakhala ku Patirosi mʼdziko la Igupto, anati kwa Yeremiya, 16 “Ife sitimvera uthenga umene watiwuza mʼdzina la Yehova! 17 Koma tidzachitadi chilichonse chimene tinanena kuti tidzachita: Tidzafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndipo tidzayipatsa nsembe yachakumwa ngati mmene tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akuluakulu mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu. Nthawi imeneyo ife tinali ndi chakudya chochuluka ndipo tinali pabwino, sitimapeza mavuto. 18 Koma kuchokera nthawi imene tinasiya kufukiza lubani ndi kupereka chopereka cha chakumwa kwa mfumukazi yakumwamba, ifeyo takhala tikusowa zinthu ndipo takhala tikuphedwa ndi lupanga ndi kufa ndi njala.”

19 Akazi anawonjezera kunena kuti, “Pamene tinkafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza mmene timayipangira mfumukazi yakumwambayo makeke abwino olembapo chinthunzi chake ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa?”

20 Yeremiya atamva kuyankha kumeneku anawawuza kuti, 21 “Kodi mukuganiza kuti Yehova nʼkuyiwala kuti inuyo ndi makolo anu, mafumu anu ndi akuluakulu anu, ndiponso anthu onse, munkafukiza lubani kwa mafano a mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? 22 Ndiye Yehova sakanathanso kupirira ndi machitidwe anu ndi zonyansa zimene munkachita. Nʼchifukwa chake dziko lanu linasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa. Dziko lopandamo anthu monga zilili lero lino. 23 Mavuto awa akugwerani chifukwa munkafukiza lubani ndipo munkachimwira Yehova pokana kumvera mawu ake ndi kutsatira malamulo ndi malangizo ake.”

24 Kenaka Yeremiya anawuza anthu onse, makamaka akazi kuti, “Imvani mawu a Yehova, anthu onse a ku Yuda amene muli mu Igupto. 25 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu ndi akazi anu munalonjeza ndi pakamwa panu, ndipo malonjezowo mwakwaniritsa. Inu munanena kuti, ‘Tidzachita zimene tinalonjeza, kufukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha zakumwa.’ Tsopano chitanitu zimene munalonjezazo! Kwaniritsani malumbiro anu.

“Yambani, chitani zimene munalonjeza! Kwaniritsani malumbiro anu! 26 Koma imvani mawu a Yehova, inu Ayuda nonse amene mukukhala mu Igupto: Yehova akuti, ‘Ine ndikulumbira mʼdzina langa lopambana kuti palibe wochokera ku Yuda amene akukhala mu Igupto amene adzatchule dzina langa polumbira kuti, ‘Pali Ambuye Yehova wamoyo.’ 27 Pakuti ndionetsetsa kuti ndiwachitire choyipa, osati chabwino. Anthu a ku Yuda amene akukhala ku Igupto adzaphedwa pa nkhondo. Ena adzafa ndi njala mpaka onse atatheratu. 28 Amene adzapulumuke ku lupanga ndi kubwerera ku dziko la Yuda kuchokera ku Igupto adzakhala ochepa kwambiri. Choncho otsala onse a ku Yuda amene anapita kukakhala ku Igupto adzadziwa kuti mawu woona ndi ati, anga kapena awo.

29 “Ine Yehova ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano. Motero mudzadziwa kuti mawu anga akuti ndidzakulangani ndi woona. 30 Yehova akuti, ‘Ine ndidzamupereka Farao Hofira mfumu ya Igupto kwa adani ake amene akufuna kumupha, monga momwe ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, mdani wake amene ankafuna kumupha.’ ”

<- YEREMIYA 43YEREMIYA 45 ->