4 “Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda, imva lonjezo ili la Yehova. Izi ndi zimene Yehova akunena za iwe: Sudzaphedwa pa nkhondo; 5 udzafera pa mtendere. Monga anthu ankafukiza lubani poyika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iwe usanalowe ufumu, choncho nawenso podzayika maliro ako adzafukiza lubani ndipo polira azidzati, ‘Kalanga, mbuye wanga!’ Ine mwini ndalonjeza zimenezi, akutero Yehova.”
6 Ndipo mneneri Yeremiya anawuza zonsezi Zedekiya mfumu ya Yuda, mu Yerusalemu. 7 Nthawi imeneyi nʼkuti gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni likuthira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda ina yotsala ya Yuda, Lakisi ndi Azeka. Imeneyi yokha ndiye inali mizinda yotetezedwa yotsala ya ku Yuda.
12 Tsono Yehova anawuza Yeremiya kuti: 13 “Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Ine ndinachita pangano ndi makolo anu pamene ndinawatulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. Ine ndinati, 14 ‘Chaka chachisanu ndi chiwiri chilichonse aliyense wa inu ayenera kumasula mʼbale wake wa Chihebri amene anadzigulitsa yekha kwa inuyo. Iyeyo amasulidwe akagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, mumulole apite mwaufulu.’ Komatu makolo anu sanandimvere kapena kusamala konse. 15 Posachedwa pomwepa inu munalapa ndi kuchita zinthu zabwino pamaso panga: Aliyense wa inu anamasula mʼbale wake. Ndipo munachita pangano pamaso panga mʼNyumba imene imadziwika ndi dzina langa kuti mudzachitadi zimenezi. 16 Koma tsopano mwasintha maganizo anu ndipo mwayipitsa dzina langa. Mwatenganso ukapolo aamuna ndi aakazi amene munawamasula aja kuti apite kumene akufuna. Mwawakakamiza kuti akhalebe akapolo anu.
17 “Nʼchifukwa chake Yehova akuti: Inu simunandimvere Ine; simunalengeze kuti abale anu amasulidwe. Chabwino! Ine ndidzakupatsani ufulu; ufulu wake ukhala wophedwa ndi nkhondo, mliri ndi njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. 18 Inu simunasunge pangano limene munachita ndi Ine. Simunasamale lonjezo limene munachita pamaso panga. Choncho ndidzakusandutsani ngati mwana wangʼombe uja amene ankamudula pawiri napita pakati pa zigawozo. 19 Amene ankadutsa pakati pa zigawozo anali atsogoleri a Yuda ndi Yerusalemu, akuluakulu a bwalo, ansembe ndi anthu onse a mʼdzikomo. 20 Onsewa ndidzawapereka kwa adani awo amene akufuna kuwapha. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo za dziko lapansi.
21 “Ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda ndi nduna zake kwa adani awo amene akufuna kuwapha, kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni limene nthawi ino layamba kubwerera mʼmbuyo. 22 Taonani, Ine ndidzawalamula, akutero Yehova, ndipo ndidzawabweretsanso ku mzinda uno. Adzathira nkhondo mzindawu, kuwulanda ndi kuwutentha. Ndipo Ine ndidzasandutsa chipululu mizinda ya Yuda kotero kuti palibe amene adzakhalemo.”
<- YEREMIYA 33YEREMIYA 35 ->