4 Patapita nthawi Aamoni anadzachita nkhondo ndi Israeli. 5 Tsono pamene Aamoni ankathira nkhondo Aisraeli, akuluakulu a ku Giliyadi anapita kukamutenga Yefita ku dziko la Tobu. 6 Iwo anati kwa iye, “Bwera ukhale mkulu wathu wankhondo kuti timenyane ndi Amoni.”
7 Yefita anawawuza Agiliyadi kuti, “Kodi inu suja munkadana nane ndi kundithamangitsa ku nyumba ya abambo anga? Nʼchifukwa chiyani lero mwabwera kwa ine pamene muli pa mavuto?”
8 Akuluakulu a ku Giliyadi aja anamuyankha kuti, “Chimene tabwerera kwa iwe ndi chakuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo udzakhala wolamulira wa onse okhala mu Giliyadi.”
9 Yefita anawayankha akuluakulu a ku Giliyadi kuti, “Ngati mundibwezeranso kwathu kuti ndikachite nkhondo ndi Aamoni ndipo Yehova nʼkukandithandiza kuwagonjetsa, ndidzakhaladi wokulamulirani?”
10 Akuluakulu a ku Giliyadi anamuyankha kuti, “Yehova akhale mboni pakati pa inu ndi ife, ngati sitidzachita monga mwa mawu anu.” 11 Choncho Yefita anapita nawo akuluakulu a ku Giliyadi aja, ndipo anthu a kumeneko anamusandutsa kukhala wowalamulira ndi mkulu wankhondo. Tsono Yefita anabwerezanso mawu omwewa pamaso pa Yehova ku Mizipa.
12 Kenaka Yefita anatuma amithenga kwa mfumu ya Aamoni ndi funso lakuti, “Kodi ife takuchimwirani chiyani kuti muzichita nkhondo ndi dziko langa?”
13 Ndipo mfumu ya Aamoni inayankha amithenga a Yefita aja kuti, “Pamene Israeli amatuluka kuchokera mu Igupto, analanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yorodani. Tsopano mundibwezere dziko langa mwamtendere.”
14 Yefita anatumizanso amithenga akewo kwa mfumu ya Aamoni 15 kukanena kuti,
29 Tsono Mzimu wa Yehova unatsikira pa Yefita. Ndipo iye ananyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Anafika ku Mizipa mʼdziko la Giliyadi, ndipo kuchokera kumeneko anapita kukalimbana ndi Aamoni. 30 Yefita analumbira kwa Yehova kuti, “Ngati mupereka Aamoni mʼmanja mwanga, 31 aliyense amene atuluke pa khomo la nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera nditagonjetsa Aamoni adzakhala wake wa Yehova, ndipo ndidzamupereka kuti akhale nsembe yopsereza.”
32 Kenaka Yefita anawolokera kwa Aamoni kukamenya nawo nkhondo, ndipo Yehova anawaperekadi mʼmanja mwake. 33 Iye anawononga mizinda makumi awiri kuchokera ku Ariori mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti. Anapitirira mpaka ku Abeli-Keranimu. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamoni.
34 Pambuyo pake Yefita anabwerera ku nyumba yake. Tsono anangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamuchingamira akuyimba ngʼoma ndi kuvina. Uyu anali mwana yekhayo wa Yefita. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35 Yefita ataona mwana wake uja, anangʼamba zovala zake ndi kulira, “Kalanga ine! Mwana wanga! Wandivulaza kwambiri ndipo iwe ndi gwero la mavuto anga. Ine ndinalumbira kwa Yehova ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro angawo.”
36 Mwanayo anayankha kuti, “Abambo, ngati munalonjeza kwa Yehova ndi pakamwa panu, chitani zimene munalonjezera pakuti Yehova wakuthandizani kulipsira adani anu Amowabu.” 37 Anatinso kwa abambo ake, “Ndikupempheni chinthu ichi: Mundilole ndikayendeyende ku mapiri miyezi iwiri ndizikalira pamodzi ndi anzanga chifukwa ndikufa ndikanali namwali wosadziwa mwamuna.”
38 Yefita anamuyankha kuti, “Pita.” Ndipo anamulola kuti apite miyezi iwiri. Tsono anapita kumapiri ndi atsikana anzake kukalira chifukwa cha unamwali wake. 39 Miyezi iwiri itatha iye anabwerera kwa abambo ake, ndipo anachitadi zimene analonjeza.