11 Yehova anawafunsa kuti, “Suja ine ndinakupulumutsani kwa Aigupto, Aamori, Aamoni ndi Afilisti? 12 Ndiponso pamene Asidoni, Aamaleki ndi Amoni anakuzunzani, inu nʼkulirira kwa ine suja ndinakupulumutsani kwa anthu amenewa? 13 Komabe inu mwandikana ndipo mukutumikira milungu ina. Choncho sindidzakupulumutsaninso. 14 Pitani kalireni kwa milungu imene mwayisankha. Iyoyo ikupulumutseni ku mavuto anuwo.”
15 Koma Aisraeli anayankha Yehova kuti, “Ife tachimwa. Tichitireni chimene mukuona kuti ndi chabwino, koma chonde tipulumutseni lero lokha.” 16 Ndipo anachotsa milungu ya chilendo pakati pawo ndi kuyamba kutumikira Yehova. Ndipo Yehova anamva chisoni poona mmene Aisraeli ankazunzikira.
17 Tsono Aamoni anasonkhana ndi kumanga zithando za nkhondo ku Giliyadi. Nawonso Aisraeli anasonkhana ndi kumanga zithando zawo za nkhondo ku Mizipa. 18 Kenaka anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi anayamba kufunsana kuti, “Kodi ndi munthu wotani amene atayambe kuthira nkhondo Aamoni? Iyeyu adzakhala mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”
<- OWERUZA 9OWERUZA 11 ->