1 Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba. 2 Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.
3 Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka. 4 Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo. 5 Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” 6 Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.