5 Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu 6 amene ankakhala ku Ahori, ku dziko la mapiri la Seiri mpaka ku Eli Parani kufupi ndi chipululu. 7 Kenaka anabwerera napita ku Eni-Misipati (ku Kadesi), ndipo anagonjetsa dera lonse la Aamaleki, kuphatikizanso Aamori amene ankakhala ku Hazazoni Tamara.
8 Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi ku Bela (ku Zowari) anapita ku Chigwa cha Sidimu kukakonzekera kuthira nkhondo 9 Kedorilaomere mfumu ya Elamu, Tidala mfumu ya Goimu, Amarafeli mfumu ya Sinara ndi Arioki mfumu ya Elasara. Mafumu anayi analimbana ndi mafumu asanu. 10 Koma Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje aphula. Choncho pamene mafumu a ku Sodomu ndi Gomora amathawa, ankhondo ena anagweramo ndipo ena anathawira ku mapiri. 11 Mafumu anayi aja anatenga katundu yense ndi chakudya chonse cha ku Sodomu ndi Gomora napita nazo. 12 Anatenganso Loti, mwana wa mʼbale wake wa Abramu pamodzi ndi katundu wake popeza ankakhala mu Sodomu.
13 Koma munthu wina amene anathawa, anabwera kudzamufotokozera Abramu Mhebri. Tsono Abramu ankakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya Mamre wa fuko la Aamori, mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri. Onsewa anali pa mgwirizano ndi Abramu. 14 Abramu atamva kuti Loti wagwidwa pa nkhondo, anasonkhanitsa asilikali 318 obadwira mʼbanja lake lomwelo nalondola mpaka ku Dani. 15 Pa nthawi ya usiku Abramu anawagawa asilikali ake kuti athire nkhondo mafumu aja, ndipo anawakantha nawapirikitsa mpaka ku Hoba, cha kumpoto kwa Damasiko. 16 Ndipo anawalanda katundu wawo yense nabwera naye Loti, katundu wake yense, pamodzi ndi akazi ndi anthu ena.
17 Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu).
18 Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku Salemu anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba, 19 ndipo anadalitsa Abramu nati,
21 Mfumu ya Sodomu inati kwa Abramu, “Ine undipatse anthu okhawo, koma katundu akhale wako.”
22 Koma Abramu anawuza mfumu ya Sodomu kuti, “Ndakweza manja anga kwa Yehova, Mulungu Wammwambamwamba, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kulumbira 23 kuti sindidzalandira kanthu kalikonse kako, ngakhale utakhala ulusi chabe kapena chingwe cha nsapato, kuopa kuti ungamanene kuti, ‘Ndamulemeretsa Abramu.’ 24 Sindidzalandira kanthu kalikonse kupatula zokhazo zimene anthu anga adya ndi gawo la katundu la anthu amene ndinapita nawo monga Aneri, Esikolo ndi Mamre. Iwowa atenge gawo lawo.”
<- GENESIS 13GENESIS 15 ->