Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
11
Nsanja ya Babeli
1 Nthawi imeneyo anthu onse a pa dziko lapansi ankayankhula chiyankhulo chimodzi ndipo mawu amene ankayankhula anali amodzi. 2 Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako.

3 Tsono anawuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuziwotcha bwinobwino.” Tsono mʼmalo mwa miyala anagwiritsa ntchito njerwa zowotcha, ndipo mʼmalo mwa matope anagwiritsa ntchito phula. 4 Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.”

5 Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. 6 Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. 7 Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.”

8 Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. 9 Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.

Mibado Kuyambira pa Semu Mpaka Abramu
10 Nayi mibado yochokera kwa Semu.
 
Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. 11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhala ndi moyo zaka 500 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

12 Pamene Aripakisadi anali ndi zaka 35, anabereka Sela. 13 Atabereka Sela, Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

14 Pamene Sela anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Eberi. 15 Atabereka Eberi, Sela anakhala ndi moyo zaka zina 403 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

16 Pamene Eberi anali ndi zaka 34 anabereka Pelegi. 17 Atabereka Pelegi, Eberi anakhala ndi moyo zaka zina 430 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

18 Pamene Pelegi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Reu. 19 Atabereka Reu, Pelegi anakhala zaka zina 209 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

20 Pamene Reu anali ndi zaka 32, anabereka Serugi. 21 Atabereka Serugi, Reu anakhala ndi moyo zaka zina 207 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

22 Pamene Serugi anali ndi zaka makumi atatu, anabereka Nahori. 23 Atabereka Nahori, Serugi anakhala ndi moyo zaka zina 200 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

24 Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. 25 Atabereka Tera, Nahori anakhala ndi moyo zaka zina 119 ndipo anali ndi ana ena aamuna ndi aakazi.

26 Pamene Tera anali ndi zaka 70, anabereka Abramu, Nahori ndi Harani.

Mibado Yochokera mwa Tera
27 Nayi mibado yochokera mwa Tera.
 
Tera anabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Ndipo Harani anabereka Loti. 28 Abambo ake a Tera akanali ndi moyo, Harani anamwalira ku Uri wa ku Akaldeya kumene anabadwira. 29 Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. 30 Sarai analibe ana chifukwa anali wosabereka.

31 Tera anatenga mwana wake Abramu, mdzukulu wake Loti, ndi mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu natuluka mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kupita ku Kanaani. Pamene anafika ku Harani, anakhazikika kumeneko.

32 Tera anamwalira ku Harani ali ndi zaka 205.

<- GENESIS 10GENESIS 12 ->