Link to home pageLanguagesLink to all Bible versions on this site
2
Mʼndandanda wa Ayuda amene Anabwerera
1 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. 2 Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).
 
Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:
   Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya) 74.
  • EZARA
  • <
  • 2
  • >