6 Munthuyo ali chiyimire pambali panga, ndinamva wina akundiyankhula kuchokera mʼNyumba ya Mulungu. 7 Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga waufumu, ndi malo opondapo mapazi anga. Pano ndiye pamene ndidzakhala pakati pa Aisraeli mpaka muyaya. Aisraeliwa kapena mafumu awo sadzayipitsa dzina langa popembedza milungu ina kapena poyika mitembo ya mafumu awo ku zitunda zachipembedzo. 8 Ankamanga chiwundo chawo pafupi ndi chiwundo changa, ndiponso mphuthu zawo pafupi ndi mphuthu zanga, nʼkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero anayipitsa dzina langa loyera ndi machitidwe awo onyansa. Choncho Ine ndinawawononga ndili wokwiya. 9 Tsopano alekeretu kupembedza milungu ina ndipo achotseretu mitembo ya mafumu awo, isakhale pafupi ndi Ine, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo mpaka muyaya.
10 “Iwe mwana wa munthu, awuze Aisraeliwa za Nyumba ya Mulunguyi, mamangidwe ake ndipo achite manyazi ndi machimo awo, 11 akachita manyazi ndi zoyipa zonse anachita, uwafotokozera za Nyumba ya Mulungu, mamangidwe ake, makomo ake otulukira ndi makomo olowera, ndiye kuti, mamangidwe ake onse. Uwafotokozerenso malangizo ndi malamulo ake. Uwalembe akuona kuti athe kuwasunga ndi kuwachita.
12 “Limeneli ndi lamulo la Nyumba ya Mulungu imene idzamangidwe pamwamba pa phiri. Malo ake onse ozungulira adzakhala oyera kwambiri. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu.
18 Kenaka munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, Ambuye Yehova akuti: Guwalo litamangidwa, tsono malamulo awa azidzatsatidwa popereka nsembe zopsereza ndiponso powaza magazi pa guwapo. 19 Udzawapatse ansembe, omwe ndi Alevi, a banja la Zadoki, amene amabwera pafupi nane kudzanditumikira, mwana wangʼombe wamwamuna kuti aperekere nsembe yopepesera machimo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 20 Udzatengeko magazi ake ena ndi kuwapaka pa nyanga zinayi za pa guwa lansembe, pa ngodya zinayi za phaka ndiponso mozungulira mkombero wonse. Motero udzaliyeretsa ndi kulipatula. 21 Udzatenge ngʼombe yayimuna yomwe yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo, ndipo udzayiwotche pa malo ake enieni mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.
22 “Mmawa mwake udzatenge mbuzi yopanda chilema kuti nayonso iperekedwe ngati nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake idzayeretse guwa lansembe monga unachitira ndi ngʼombe yayimuna ija. 23 Utatha kuyeretsa guwa lansembelo, udzatenge mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndiponso nkhosa yayimuna yopanda chilema. 24 Udzapereke zonsezi pamaso pa Yehova, ndipo ansembe adzazithire mchere ndi kuzipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Yehova.
25 “Kwa masiku asanu ndi awiri, uzidzapereka tsiku ndi tsiku mbuzi yayimuna, mwana wangʼombe, ndiponso nkhosa kuti zikhale nsembe zopepesera machimo. Zonsezi zidzakhale zopanda chilema. 26 Kwa masiku asanu ndi awiriwo ansembe adzachite mwambo woyeretsa ndi kupatula guwa lansembelo. 27 Masiku amenewa atatha, kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu, ansembe azipereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe. Apo ndidzakulandirani. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
<- EZEKIELI 42EZEKIELI 44 ->