7 “ ‘Konzekani! Mukhaledi okonzeka, iweyo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo limene lakusonkhanira. Iweyo udzawatsogolera pokamenya nkhondo. 8 Pakapita masiku ambiri ndidzakuyitana. Zaka zikubwerazi ndidzakulowetsa mʼdziko limene lapulumuka ku nkhondo. Anthu ake anasonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu ya anthu ambiri nʼkukakhazikika pa mapiri a Israeli amene kwa nthawi yayitali anali ngati chipululu. Anthu onsewa tsopano akukhala mwa mtendere. 9 Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse ndiponso mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mitambo.
10 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limenelo mu mtima mwako mudzabwera maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoyipa. 11 Iwe udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda mipanda; ndikathira nkhondo anthu okhala mwamtendere, anthu amene satchinjirizidwa ndi mipanda, zipata kapena mipiringidzo. 12 Ndipita kukalanda chuma chawo ndi kukafunkha zinthu zawo. Ndidzalimbana ndi midzi imene kale inali mabwinja. Ndikathira nkhondo anthu amene anasonkhanitsidwa kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Iwowa ali ndi ziweto zambiri, katundu wochuluka ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’ 13 Anthu a ku Seba, a ku Dedani ndiponso amalonda a ku Tarisisi pamodzi ndi midzi yake yonse adzakufunsa kuti, ‘Kodi wabwera kudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako la nkhondo kudzalanda chuma, kudzatenga siliva ndi golide, ziweto ndi katundu kuti zikhale zofunkha zochuluka?’ ”
14 “Nʼchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, nenera ndipo uwuze Gogi kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene anthu anga adzakhala pa mtendere, iwe udzanyamuka. 15 Udzabwera kuchokera ku dziko lako kutali kumpoto, iwe pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, onse okwera akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu. 16 Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraeli ngati mtambo wophimba dziko. Masiku amenewo, iwe Gogi, ndidzabwera nawe kuti ulimbane ndi dziko langa, kuti anthu a mitundu ina andidziwe Ine, pamene ndidzaonetsa kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo.
17 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi iwe si amene ndinayankhula za iwe masiku amakedzana kudzera mwa atumiki anga aneneri a Israeli? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzawutsa iwe kuti udzalimbane ndi Israeli. 18 Zimene chidzachitika pa tsiku limenelo ndi izi: Gogi akadzathira nkhondo dziko la Israeli, mkwiyo wanga woopsa udzayaka. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. 19 Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo Ine ndikunenetsa kuti pa nthawi imeneyo padzakhala chivomerezi chachikulu mʼdziko la Israeli. 20 Nsomba za mʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zirombo zakuthengo, cholengedwa chilichonse chimene chimakwawa pansi, ndiponso anthu onse okhala pa dziko lapansi, adzanjenjemera pamaso panga. Mapiri adzangʼambika, malo okwera kwambiri adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi. 21 Ndidzawutsira Gogi nkhondo kuchokera ku mapiri anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga. 22 Ine ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ya matalala, ndiponso sulufule ndi miyala ya moto pa iye ndi pa asilikali ake ndiponso pa mitundu yambiri ya anthu imene ili naye. 23 Motero ndidzadzionetsa kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Ndiponso ndidzadziwika pamaso pa anthu a mitundu ina yambiri. Momwemo adzadziwadi kuti Ine ndine Yehova.’ ”
<- EZEKIELI 37EZEKIELI 39 ->