1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Taona ine ndakuyika kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mʼbale wako Aaroni adzakhala mneneri wako. 2 Iwe ukanene zonse zimene ndakulamulirazi, ndipo Aaroni mʼbale wako ndiye akaziyankhule kwa Farao kuti atulutse ana a Israeli mʼdziko la Igupto. 3 Koma ndidzawumitsa mtima wa Farao, ndipo ngakhale nditachulukitsa zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa mu Igupto, 4 iyeyo sadzakumverani. Choncho ndidzakantha Igupto, ndipo ndi ntchito zachiweruzo ndidzatulutsa magulu anga, anthu anga Aisraeli kuwachotsa mʼdziko la Igupto. 5 Ndipo Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzatambasula dzanja langa kukantha Igupto ndi kutulutsa Aisraeli mʼdzikomo.”
6 Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova anawalamulira. 7 Mose anali ndi zaka 80, ndipo Aaroni anali ndi zaka 83 pamene anakayankhula kwa Farao.
10 Kotero Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kuchita monga momwe Yehova anawalamulira. Aaroni anaponya ndodo yake pansi patsogolo pa Farao ndi nduna zake ndipo inasanduka njoka. 11 Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. 12 Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo. 13 Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.
19 Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.”
20 Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova analamulira. Anakweza ndodo yake pamaso pa Farao ndi akuluakulu ake ndipo anamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi. 21 Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto.
22 Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu. 23 Mʼmalo mwake iye anatembenuka ndi kupita ku nyumba yake yaufumu ndipo zimenezi sanazilabadire. 24 Anthu onse a ku Igupto anayamba kukumba mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sanathe kumwa madzi a mu mtsinjemo.