Deuteronomo
3 Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo. 4 Apa nʼkuti atagonjetsa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni, ndipo pa Ederi anagonjetsa Ogi mfumu ya ku Basani, amene amalamulira mu Asiteroti.
5 Chakummawa kwa Yorodani mʼchigawo cha Mowabu, Mose anayamba kufotokozera lamulo ili kunena kuti:
14 Inu munandiyankha kuti, “Maganizo amenewa ndi abwino kuwachita.”
15 Choncho ndinatenga anthu otsogolera mafuko anu, anzeru ndi omwe mumawalemekeza, ndipo ndinawayika kuti azikulamulirani mʼmagulu a 1,000, ena 100, ena makumi asanu ndi ena khumi, kuti akhalenso ngati akapitawo a mafuko. 16 Ndipo pa nthawi imeneyo ndinawawuza olamula anu kuti, “Muzimva milandu ya pakati pa abale anu ndi kuweruza mosakondera, kaya mlanduwo uli pakati pa Aisraeli okhaokha kapena mmodzi wa iwo ndi mlendo. 17 Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.” 18 Ndipo nthawi imeneyo ndinakuwuzani chilichonse chimene munayenera kuchita.
22 Tsono nonse munabwera kwa ine ndi kuti, “Tiyeni titumize anthu ayambe apita kuti akazonde dzikolo ndi kutibweretsera mawu pa za njira yomwe tidzere ndi za mizinda imene tikafikireko.”
23 Ndinaona kuti maganizo amenewa anali abwino, choncho ndinasankha anthu khumi ndi awiri, mmodzi ku fuko lililonse. 24 Iwo ananyamuka napita mʼdziko la mapiri, ndipo anafika ku Chigwa cha Esikolo ndi kukazonda dzikolo. 25 Pobwerera anatitengerako zipatso za mʼdzikomo ndipo anatipatsa mawu akuti, “Dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa ndi labwino.”
29 Ndipo ine ndinati kwa inu, “Musachite mantha kapena kuwaopa. 30 Yehova Mulungu wanu, amene akukutsogolerani, adzakumenyerani nkhondo monga muja anachitira ku Igupto inu mukuona, 31 ndi mʼchipululu muja. Kumeneko munaona mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani monga abambo anyamulira mwana wawo, njira yonse yomwe munayenda mpaka munafika pamalo ano.”
32 Ngakhale zinali choncho, simunadalire Yehova Mulungu wanu 33 amene anakutsogolerani pa ulendo wanu, ndi moto nthawi ya usiku ndi mtambo nthawi ya masana, kukufunirani malo woti mumange msasa ndi kukuonetsani njira yoti muyendemo.
34 Yehova atamva zimene munanena anakwiya nalumbira kuti, 35 “Palibe ndi mmodzi yemwe mwa mʼbado woyipawu amene adzaona dziko labwino limene ndinalumbira kupatsa makolo anu, 36 kupatula Kalebe mwana wa Yefune. Iye adzaliona, ndipo ndidzamupatsa iye ndi adzukulu ake, dziko limene adzapondamo popeza anatsata Yehova ndi mtima wake wonse.”
37 Chifukwa cha inu, Yehova anakwiyiranso ine ndipo anati, “Iwenso sudzalowa mʼdzikomo. 38 Koma Yoswa mwana wa Nuni amene amakuthandiza, adzalowa mʼdzikomo. Umulimbikitse chifukwa adzatsogolera Israeli kukalandira dzikolo. 39 Ndipo angʼonoangʼono amene munati adzagwidwa ukapolo, ana anu amene sanadziwe kusiyanitsa chabwino ndi choyipa, amenewo adzalowa mʼdzikolo. Ndidzalipereka kwa iwo ndipo lidzakhala lawo. 40 Koma inu, tembenukani nyamukani kulowera cha ku chipululu kutsatira njira ya ku Nyanja Yofiira.”
41 Ndipo inuyo munati, “Tachimwa pamaso pa Yehova. Tipita ndi kukachita nkhondo monga Yehova Mulungu wathu watilamulira.” Choncho aliyense wa inu anavala zankhondo, ndi kuganiza kuti nʼkosavuta kupita mʼdziko la mapiri lija.
42 Koma Yehova anandiwuza kuti, “Awuze anthuwa kuti, ‘Musapite kukachita nkhondo chifukwa Ine sindidzakhala nanu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu.’ ”
43 Choncho ndinakuwuzani koma simunamve. Inu munawukira lamulo la Yehova ndipo mwamwano munayenda kulowa mʼdziko la mapiri. 44 Aamori amene ankakhala mʼmapiriwo anatuluka kukakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati gulu la njuchi ndipo anakukanthani kuchokera ku Seiri, njira yonse mpaka ku Horima. 45 Munabwererako mukulira pamaso pa Yehova, koma Iye sanalabadire kulira kwanuko ndipo sanakumvetsereni. 46 Pamenepo munakhala ku Kadesi masiku ambiri kwa nthawi yayitali ndithu.
DEUTERONOMO 2 ->