1 Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene. 2 Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
3 Kotero Yehova anakhululuka.
Yehovayo anati, “Izi sizidzachitika.”
4 Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko. 5 Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
6 Kotero Yehova anakhululuka.
Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.”
7 Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma. 8 Ndipo Ambuye anandifunsa kuti, “Amosi, nʼchiyani ukuonachi?”
Ine ndinayankha kuti, “Chingwe chowongolera khoma.”
Ndipo Yehova anati, “Taona, Ine ndikuyika chingwe chowongolerachi pakati pa anthu anga, Aisraeli; sindidzawalekereranso.
9 “Malo achipembedzo a Isake adzawonongedwa
ndipo malo opatulika a Israeli adzasanduka bwinja;
ndidzagwetsa nyumba ya Yeroboamu ndi lupanga langa.”
Amosi ndi Amaziya
10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo. 11 Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi:
“ ‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga,
ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo,
kutali ndi dziko lake.’ ”
12 Ndipo Amaziya anawuza Amosi kuti, “Choka, mlosi iwe! Bwerera ku dziko la Yuda. Uzikalosera kumeneko ndipo anthu a kumeneko azikakudyetsa. 13 Usanenerenso ku Beteli, chifukwa kumeneko ndi malo opatulika a mfumu ndiponso ndi malo a nyumba yachipembedzo yaufumu.”
14 Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu. 15 Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’ 16 Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti,
“ ‘Usanenere zotsutsa Israeli,
ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ”
17 “Tsono zimene akunena Yehova ndi izi:
“ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu,
ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga.
Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa,
ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu.
Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,