1 Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita. 2 Anthu a pa chilumbacho anatichitira zokoma zimene sizichitika kawirikawiri. Iwo anakoleza moto natilandira tonse chifukwa kumagwa mvula ndipo kumazizira. 3 Paulo anatola mtolo wankhuni, pamene amayika pa moto, munatulukamo njoka chifukwa cha kutentha, ndipo inamuluma pa dzanja. 4 Anthu a pa chilumbacho ataona njokayo ili lende pa dzanja lake, iwo anawuzana kuti, “Munthu uyu akuyenera kukhala munthu wopha anthu; pakuti ngakhale wapulumuka pa nyanja, chilungamo sichinamulore kuti akhale ndi moyo.” 5 Koma Paulo anayikutumulira pa moto njokayo, ndipo sanamve kupweteka. 6 Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu.
7 Pafupi ndi malowa panali munda wa Popliyo, mkulu wa boma la pa chilumbacho. Iye anatilandira natisamala bwino masiku atatu. 8 Abambo ake anali gone, chifukwa amadwala malungo ndi kamwazi. Paulo analowa mʼchipinda chake kukawaona, ndipo atapemphera, anasanjika manja ake pa iwo nawachiritsa. 9 Zitachitika zimenezi, anthu onse odwala a pa chilumbacho anabwera ndipo anachiritsidwa. 10 Anthuwo anatilemekeza ife mʼnjira zambiri ndipo pamene tinakonzeka kuti tiyambe ulendo, anatipatsa zonse zomwe tinazisowa.
Paulo Afika ku Roma
11 Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pa sitima ina imene inakhala pa chilumbacho chifukwa cha kuzizira. Inali sitima ya ku Alekisandriya imene inali ndi chizindikiro cha milungu ya mapasa yotchedwa Kastro ndi Polikisi. 12 Tinakafika ku Surakusa ndipo kumeneko tinakhalako masiku atatu. 13 Kuchokera kumeneko tinayenda ndi kukafika ku Regio. Mmawa mwake mphepo yochokera kummwera inawomba, ndipo tsiku linalo tinakafika ku Potiyolo. 14 Kumeneko tinapezako abale amene anatiyitana kuti tikhale nawo sabata limodzi. Ndipo kenaka tinapita ku Roma. 15 Abale kumeneko atamva kuti tikubwera, anabwera kudzakumana nafe mpaka ku bwalo la Apiyo ndiponso ku nyumba za alendo zitatu. Atawaona anthu amenewa Paulo anayamika Mulungu ndipo analimbikitsidwa. 16 Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kukhala pa yekha ndi msilikali womulondera.
Paulo Alalikira kwa Ayuda ku Roma
17 Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa pamodzi atsogoleri a Ayuda. Atasonkhana, Paulo anawawuza kuti, “Abale anga, ngakhale kuti ine sindinachite kanthu kalikonse kulakwira mtundu wathu kapena miyambo ya makolo athu, koma anandigwira mu Yerusalemu ndi kundipereka mʼmanja mwa Aroma. 18 Iwo anandifufuza ndipo anafuna kundimasula chifukwa sanandipeze wopalamula mlandu woyenera kuphedwa. 19 Koma Ayuda atakana, ine ndinakakamizidwa kupempha kuti ndikaonekere pamaso pa Kaisara, sikuti ndinali ndi kanthu konenezera mtundu wanga. 20 Pa chifukwa ichi ndapempha kuti ndionane nanu ndi kuyankhula nanu. Pakuti nʼchifukwa cha chiyembekezo cha Israeli ndamangidwa unyolo uwu.”
21 Iwo anayankha kuti, “Ife sitinalandire kalata iliyonse yochokera ku Yudeya yonena za iwe, ndipo palibe mmodzi wa abale amene anachokera kumeneko anafotokoza kapena kunena kalikonse koyipa ka iwe. 22 Koma ife tikufuna kumva maganizo ako ndi otani, pakuti tikudziwa kuti ponseponse anthu akuyankhula zotsutsana ndi mpatuko umenewu.”
23 Iwo anakonza tsiku lina loti akumane ndi Paulo, ndipo anabwera anthu ambiri ku nyumba kumene amakhala. Kuyambira mmawa mpaka madzulo, Paulo anawafotokozera ndi kuwawuza za ufumu wa Mulungu ndipo anayesa kuwakopa kuti akhulupirire Yesu kuchokera mʼMalamulo a Mose ndiponso mʼmabuku a Aneneri. 24 Ena anakopeka ndi zimene Paulo ananena, koma enanso sanakhulupirire. 25 Ndipo anayamba kuchoka popeza sanagwirizane pakati pawo Paulo atanena mawu awa omaliza akuti, “Mzimu Woyera anayankhula zoona za makolo anu pamene Iye ananena kudzera mwa Mneneri Yesaya kuti,
26 “Pita kwa anthu awa ndi kuwawuza kuti,
‘Kumva mudzamva, koma osamvetsetsa;
kupenya mudzapenya, koma osaona kanthu.’
27 Pakuti mtima wa anthu ndi wokanika;
mʼmakutu mwawo ndi mogontha,
ndipo atsinzina kuti asaone kanthu.
Mwina angapenye ndi maso awo,
angamve ndi makutu awo,
angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,
Ineyo nʼkuwachiritsa.
28 “Chifukwa chake ine ndikufuna mudziwe kuti chipulumutso cha Mulungu chatumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzamvera.” 29 Paulo atanena mawu amenewa, Ayuda aja anachoka akutsutsana kwambiri.
30 Paulo anakhala kumeneko zaka ziwiri zathunthu mʼnyumba yobwereka yomwe amalipira ndipo ankalandira aliyense amene amabwera kudzamuona. 31 Molimba mtima ndi popanda womuletsa, Paulo analalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.