7 Iye anatenga fano losema la Asera limene analipanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Yehova, Nyumba imene Yehova ananena kwa Davide ndi mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba iyi ndi mu Yerusalemu ndiwo malo amene ndasankha pakati pa mafuko onse a Aisraeli kuyikamo Dzina langa kwamuyaya. 8 Sindidzalola kuti Aisraeli achotsedwe mʼdziko lawo limene ndinapatsa makolo awo ngati iwowo adzasamala kuchita zinthu zonse zimene ndinawalamula ndi kusunga malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anawapatsa.” 9 Koma anthu sanamvere. Manase anawasocheretsa, kotero kuti anachita zoyipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Yehova anawawononga pamene Aisraeli ankafika.
10 Yehova anayankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri kuti, 11 “Manase mfumu ya Yuda wachita machimo onyansawa ndipo wachita zoyipa kupambana Aamori amene analipo kale iye asanabadwe ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda ndi mafano ake. 12 Choncho Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taonani, ndikubweretsa pa Yerusalemu ndi Yuda mavuto akuti aliyense amene adzawamve adzathedwa nzeru. 13 Ndidzalanga Yerusalemu ndi Yuda pogwiritsa ntchito muyeso umene ndinalangira Samariya ndi Ahabu pamodzi ndi nyumba yake. Ndidzayeretsa Yerusalemu monga mmene munthu amachitira popukuta mbale ndipo atayipukuta amayivundikira pansi. 14 Ndidzawataya anthu otsala amene ndi cholowa changa ndipo ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo. Adzachotsedwa ndipo adaniwo adzawalanda zinthu zonse 15 chifukwa anachita zoyipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuchokera tsiku limene makolo awo anatuluka mu Igupto mpaka lero lino.’ ”
16 Kuwonjezera apo, Manase anakhetsa kwambiri magazi a anthu osalakwa mpaka magaziwo kuyenderera mu Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina, kuphatikiza pa kuchimwitsa Yuda, kotero kuti anthu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
17 Ntchito zina za Manase ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 18 Manase anagona ndi makolo ake ndipo anayikidwa mʼmanda mʼmunda wa Uza, ku nyumba yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
23 Nduna za Amoni zinamuchita chiwembu ndipo zinamupha mʼnyumba yake. 24 Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anachitira chiwembu Mfumu Amoni, nayika Yosiya mwana wake kukhala mfumu mʼmalo mwake.
25 Ntchito zina za Amoni ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 26 Iye anayikidwa mʼmanda ake mʼmunda wa Uza. Ndipo Yosiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
<- 2 MAFUMU 202 MAFUMU 22 ->