1 Kotero ndinatsimikiza maganizo anga kuti ndisachitenso ulendo wina owawa wobwera kwanuko. 2 Pakuti ngati ndikumvetsani chisoni, kodi angandisangalatse ndani, kupatula inuyo amene ndakumvetsani chisoni? 3 Nʼchifukwa chake ndinakulemberani monga ndinachitiramo kuti nditabwera kwanuko ndisadzamve chisoni ndi anthu oyenera kundisangalatsa. Ndinali ndi chikhulupiriro ndi inu nonse kuti inuyo mukakhala ndi chimwemwe poona kuti inenso ndili ndi chimwemwe. 4 Pakuti ndinakulemberani kalata ija ndili wopsinjika ndi wowawidwa mtima kwambiri ndi kutuluka misozi yambiri, osati pofuna kukumvetsani chisoni koma kuti ndikudziwitseni kuti ndimakukondani kwambiri.
14 Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino. 15 Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka. 16 Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi? 17 Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.
<- 2 AKORINTO 12 AKORINTO 3 ->