1 Nʼchifukwa chake pamene sitinathenso kupirira, tinaganiza kuti kunali bwino kuti atisiye tokha ku Atene. 2 Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu, 3 ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi. 4 Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi. 5 Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula.
11 Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko. 12 Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu. 13 Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.
<- 1 ATESALONIKA 21 ATESALONIKA 4 ->