Yeteri, Meredi, Eferi ndi Yaloni. Mmodzi mwa akazi a Meredi anabereka Miriamu, Samai ndi Isiba abambo ake a Esitemowa. 18 (Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yaredi abambo ake a Gedori, Heberi abambo ake a Soko ndi Yekutieli abambo a Zanowa). Awa anali ana a mwana wamkazi wa Farao, Bitia, amene Meredi anakwatira.
19 Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wa Nahamu anali awa:
abambo ake a Keila wa ku Garimi ndi Esitemowa wa ku Maaka.
20 Ana a Simeoni anali awa:
Amnoni, Rina, Beni-Hanani ndi Tiloni.
Ana a Isi anali awa:
Zoheti ndi Beni-Zoheti.
21 Ana a Sela mwana wa Yuda anali awa:
Eri amene anabereka Leka, Laada amene anabereka Maresa ndi mabanja a anthu owomba nsalu zofewa ndi zosalala a ku Beti-Asibeya, 22 Yokimu, anthu a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi, amene ankalamulira Mowabu ndi Yasibu-Lehemu. (Nkhani zimenezi ndi zakalekale). 23 Iwo anali owumba mbiya amene ankakhala ku Netaimu ndi Gederi. Ankakhala kumeneko ndi kumatumikira mfumu.
Simeoni
24 Ana a Simeoni anali awa:
Nemueli, Yamini, Yaribu, Zera ndi Sauli;
25 Salumu anali mwana wa Sauli, Mibisamu anali mwana wa Salumu ndipo Misima anali mwana wa Mibisamu.
26 Zidzukulu za Misima zinali izi:
Hamueli, Zakuri ndi Simei.
27 Simei anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake sanabereke ana ambiri; kotero banja lawo silinakule ngati anthu ena a ku Yuda. 28 Iwo amakhala ku Beeriseba, Molada, Hazari-Suwali, 29 Biliha, Ezemu, Toladi, 30 Betueli, Horima, Zikilagi, 31 Beti-Marikaboti, Hazari-Susimu, Beti-Biri ndi Saaraimu. Iyi inali mizinda yawo mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Davide. 32 Midzi yowazungulira inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, midzi isanu 33 ndi midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baala. Awa anali malo awo okhalapo. Ndipo anasunga mbiri ya makolo awo.
34 Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya, 35 Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asieli, 36 komanso Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya, 37 ndiponso Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya.
38 Anthu amene atchulidwawa anali atsogoleri a mabanja awo. Mabanja awo anakula kwambiri 39 ndipo anakafika ku malire a Gedori ku chigwa cha kummawa kufuna msipu wodyetsa ziweto zawo. 40 Anapeza msipu wobiriwira ndi wabwino ndipo dziko linali lalikulu, la mtendere ndi bata. Kumeneko kunkakhala fuko la Hamu poyamba.
41 Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo. 42 Ndipo anthu 500 a fuko la Simeoni, motsogozedwa ndi Pelatiya, Neariya, Refaya ndi Uzieli, ana a Isi, analanda dziko lamapiri la Seiri. 43 Iwo anapha Aamaleki otsala amene anali atapulumuka ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino.